Anjatidwa Pambuyo Pogagada Ndi Kupha Mkazi Wake ndi Mpini

Mkulu wina ku Makanjira m’boma la Mangochi amuthira zingwe ati kamba koti anagagada ndi kupha mkazi wake ku Makanjira m’boma la Mangochi kamba ka nsanje, Mraravi Express yamvetsedwa motere.
Malinga ndi kunena kwa bambo Phiri omwe anaonekera ku ofesi ya Maravi Express kudzatsindika za nkhaniyi, mkuluyo akuti wakhala akukayikira ndi mayendedwe a mkazi wakeyo.
Tsiku lina mkuluyo atachoka pakhomopo akuti anatsinidwa khutu ndi anzake kuti adawona mkazi wakeyo ali ndi njonda ina ndipo izi zinamukwiyitsa kwambiri ndipo sanachedwe koma kutsatira maiyo.
Atakumana mkuluyo akuti anatenga mpini wa khasu nkuphwasamula mutu wa mkaziyo yemwe anagwa mpakana kufera pomwepo.
Atazindikila kuti mkaziyo wataya moyo wake, mkuluyo akuti anathawira ku phiri lina loyandikila kumeneko koma kenaka anabweleranso m’mudzimo kamba koti mutu wake umakhala ngati sumagwira.
Anthu m’mudzimo atamuona sanachedwe koma kumugwira ndikupita naye ku polisi komwe anamuponyera mu chitokosi.
Padakali pano, mkulu wa nkhanzayo akuyembekezeka kukawonekera ku khoti la malamulo masiku akudzawa komwe akuyembekezeka kukalandira chilango chokhwima kwambiri .
Amabiri okhudzidwa ndi nkani ngati izi amalandira chilango chokakhala kundende moyo wawo wonse.
Nkhanza kwa amayi ngakhalenso kwa abambo zakhaka zikukulirakulira m’madera ambiri mdziko muno.