Mtsikana Woyendayenda Asanduka Chinjoka kamba kobera Munthu K40,000

Pali kunena kokuti gonthi samamva kamba kakuti nkhani yomwe Maravi Express Yamvetsedwa ndi yochititsa mantha komanso yomvetsa chisoni kwa ena atsikana omwe safuna kumvela makolo koma kulowa mchitidwe woyendayenda.
Nkhaniyi ikuti atsikana awiri anatengana ku Bangula m’boma la Nsanje nkupita ku dziko la Mozambique komwe amakapanga zawo zoyendayenda.
Ndiye akuti ali kumeneko, m’modzi mwa asungwanawo anakumana ndi mamuna wina yemwe anagwirizana naye kuti akapange za dama pa in amwa nyumba zogona alendo kumeneko.
“Zitatere mzake wa donayo anadikilira koma anali odabwa kamba koti winayo samatulukira. Apa mamunayo akuti anauza mzakeyo kuti waberedwa K40,000 koma mayi woyendayendayo anakana kwantu wa galu kuti palibe china chilichonse chomwe amadziwa,” Anauza Maravi Express a Daudi omwe nkhaniyi inawachitikira maso ndi maso.
Iwo anapitilira nkunena kuti kenaka atawona kuti nthawi ikutha, mzakeyo analowa mchipinda chogona alendocho koma atangolowa anadabwa powona kuti mzakeyo anali ngati munthu mutu okha koma thupi lonse linasanduka Chinjoka.
Zitatere mzakeyo anathawa ndipo masiku enawo anthu kumeneko makamaka pa makina aja a pa Internet akuti akhala akujambula Chinjokacho chili mthengo.
Padakali pano, mzake mwa msungwanayo yemwe pano ali ku Bangula anatchayila thenifolo mkulu wake yemwe amakhala kuno ku Blantyre kumuuza za nkhaniyi koma akuti atamuuza ananenetsa kuti alibe nazo ntchito
Iyeakuti ananenetsa kuti sakumvana ndi izi kamba amafunitsitsa kuti akanasanduka m’bale wakeyo kamba koti samva malangizo kuchokera kwa akuluakulu akamuuza maka kumbali ya nkhani zoyendayenda.